Apolisi m’boma la Balaka alangiza anthu oyendetsa galimoto kuti adzigwiritsa ntchito zizindikiro zapanseu pofuna kupewa ngozi.
Apolisiwa apereka langizoli msungwana wazaka khumi ndi zitatu ndi bambo wazaka 41 atamwalila pamene adawombedwa ndi galimoto pamseu wa Mangochi- Liwonde
Mneneri wa apolisi m’bomalo Sub-Inspector Joseph Sauka,anawuza Radio Maria Malawi kuti msungwanayo wamwalira lachiwiri sabata ino galimoto la lamtundu wa Toyota Pick-Up, litamuwomba dalayivala wake atalephera kuliwongolera chifukwa chothamanga kwambiri.
Padakali pano oyendetsa galimoto lomwe lapha msungwanayo Kelvin Sambo, ali mmanja mwa apolisi ku Balaka komwe akuyembekezeka kuyankha mulandu wakupha komanso kuvulaza anthu awiri pangoziyi chifukwa choyendetsa galimoto mosasamala.
Kelvin Sambo,amachokela mmudzi mwa Chigudu mdera lamfumu yayikulu Nsakambewa m’boma la Dowa, ndipo msungwana yemwe wamwalira pa ngoziyi ndi Fanny Chikowi wammudzi mwa Phombeya mdera la mfumu yayikulu Chanthunya m’boma la Balaka.
Padakali pano anthu awiri omwe avulala pa ngoziyi akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha boma ku Machinga.