Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

KWAYA ZIZAMITSE LUSO LOPEKA NYIMBO KUCHOKERA M'BUKU LOYERA

$
0
0

M’modzi mwa akatswiri poyimba nyimbo za uzimu m’dziko muno, PAUL BANDA wati mayimbidwe mu mpingo wakatolika, angapite patsogolo komanso kuyenda bwino, pokhapokha magulu oyimba  mu mpingowu atazamitsa luso lomapeka  nyimbo zawo kuchokera  m’buku  Loyera.

Paul Banda, wati kwanthawi, yayitali tsopano magulu oyimba mu mpingo wakatolika, akhala akungokopera mayimbidwe a magulu oyimba akunja mkumatulutsa zimbale, mchitidwe womwe wakhala ukubwezeretsa  m’mbuyo luso la mayimbidwe m`magulu oimba ambiri a mpingowu m’dziko muno. Iye wayamikira kwaya zomwe zafika pa mlingo wotha kumapeka zokha nyimbo, atazindikira kuipa kongokopera luso la kwaya zina zomwe zkuchita bwino.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>