Bungwe la abwenzi a amalitiri aku Uganda lati zokonzekera za ulendo wokayendera malo oyera a Namugongo omwe amalitiri anaphedwera m’dziko la Uganda chaka chino zayenda bwino.
Malinga ndi wapampando wa bungwe la abwenzi a amalitiri a ku Uganda m’dziko muno Mai Florence Musasa abwenziwa anyamuka lachisanu pambuyo pa nsembe za ukarisitiya zomwe anali nazo m’madayosizi awo,
“Madayosizi onse m’dziko muno atumiza nthumwi zawo kupita ku ulendowu kupatulapo dayosizi ya Dedza ndipo pa ulendowu tili ndi a episkopi a dayosizi ya Mangochi Ambuye Montfort Stima, ansembe 6 ndi asisteri 6 ndipo akhristu eni ake tilipo 79,” anatero Mai Musasa.
Iwo ati chosangalatsa kwambiri ndi choti chaka chino ali ndi ana omwe anthu akufuna kwabwino awalipilira.
Mai Musasa ati kupatula kukachita nawo nsembe ya ukaristia pa 3 June ku Namugongo, azikhala ndi nsembe za ukaristia paliponse pamene aziyima kuyambira ku Tanzania komwe agoneko masiku awiri pokonzekera chaka cha Amaritiri chi.
“Tikakafika ku uganda ko, tikayendera malo osiyanasiyana. Tinamva kuti amaritiri sanaphedwere ku Namugongo kokha choncho tikafika ku malo otchedwa Munyonyo kumenenso kunaphedwa amaritiri ochuluka, tikakhalanso maphunziro osiyanasiyana a za uzimu ku Emausi komwe tikafikire kwa masiku awiri ,” anatero Mai Musasa.