Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la CCJP Lipempha Boma Lilipire Msanga Aphunzitsi ku Nsanje

$
0
0

Bungwe la chilungamo ndi mtendere mu dayosizi ya Chikwawa ya mpingo wakatolika yapempha boma kuti likonze msanga malipiro a aphunzitsi a m’boma la Nsanje omwe mpaka pano sanalandire malipiro awo a mwezi watha.

Mlembi wa bungweli a Lewis Msiyadungu ayankhula izi ndi Radio Maria Malawi, ofesi yawo italandira madandaulo kwa aphunzitsiwa.

A Msiyadungu ati aphunzitsi pafupifupi 560 ndi omwe akhudzidwa ndi vutoli zomwe zabweretsa ntchito yopereka maphunziro a pamwamba m’bomali kamba ka ndondomeko yowerengeranso aphunzitsi yomwe unduna wa zamaphunziro wachita.

“Vuto limeneli lakhuza miyoyo ya tsiku ndi tsiku ya aphunzitsiwa chifukwa ena amakhala nyumba za renti ndipo atha kuthamangitsidwa komanso aphunzitsiwa akusowa chakudya komanso akulephera kusamalira mabanja ndi abale awo,” anatero a Msiyadungu.

A Msiyadungu ati vutoli lakhuza maphunziro m’bomali chifukwa aphunzitsiwa akusiya kuphunzitsa ndi kukafunafuna ndalama zoti agulire chakudya ndi kuthandizira mabanja awo.

Radio Maria Malawi inalephera kuyankhula ndi mlembi wa unduna wa zamaphunziro, a Manifred Ndobvi, kuti athilirepo ndemanga pa nkhaniyi kaamba koti samayankha lamya.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>