Achinyamata omwe ali pamaphunziro aunsembe ku sukulu ya Kachebere m’boma la Mchinji, ayamikira gulu la amai la Chitemwano la mparishi ya St Denis ya mpingo wakatolika mudayosizi ya Mzuzu yampingowu, kaamba ka thandizo lomwe gululi lapereka kwa chinyamatawo.
Gululi lapeka ndalama zokwana 52 sauzande kwacha,paulendo omwe linakonza okayendera achinyamatawo kusukuluyo.Mlembi wamkulu wa Aseminowo Francisco Hau, wati kuchezeredwa kwao ndi amaiwo, kuwalimbikitsa kwambiri pamaphunziro awo pomwe akupitiliza maphunziro awo ofuna kudzakhala atsogoleri mumpingowu.Kuphatikiza pa ndalamazo,amaiwo aperekanso mphatso zosiyanasiyana kwa aseminowo, zomwe ati ziwathandiza munjira zosiyanasiyana.