Anthu omwe akhala akuchita kafukufuku wa ndege yomwe inasowa m’chaka cha 2014 ati apeza chidutswa cha ndegeyo m’dziko la Mozambique.
Ndegeyo yomwe nambala yake inali MH370 yomwe imachokera ku Kuala Lumpur mdziko la Malaysia kupita mu mzinda wa Beijing mdziko la China ndipo pa nthawi yosowayo inali itanyamula anthu okwana 239.
Malipoti a wailesi ya BBC ati pali zizindikiro zoti ndegeyi inasowa kum’mwera kwa nyanja yaikulu ya India. Padakali pano anthu ochita kafukufuwa akuyembekezera kupima chidutswacho ngati chili cha ndegeyo.