Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisko anakumana ndi Pulezidenti wa dziko la Costa Rica a Luis Guillermo Solis komwe anakambirana za ubale wa pakati pa dzikoli ndi likulu la mpingo wakatolika.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican pa mkumanowu Pulezidenti Solis anayamikira mpingowu mdziko la Costa Rica kaamba kotengapo gawo pa nkhani zamaphunziro, umoyo ngakhalenso ntchito zachifundo.
Atsogoleriwa ati anakambirananso nkhani zokhudza chitetezo chabwino kwa anthu, nkhani zokhudza anthu othawa kwao komanso mchitidwe wozembetsa anthu.