Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisko wapempha akhristu kuti apemphelere tsiku la pa 1 June lomwe ndi tsiku lokumbukira ana pa dziko lonse, mwapadera pokumbukira ana a mdziko la Syria.
Papa amalankhula izi ku likulu la mpingowu pa bwalo la St Peters pomwe amalandira atumiki omwe anasankha kukhala ma dikoni pamene amachita chaka chawo.
Polankhula pa nkhani yokumbukira tsiku la anali, Papa wati ndi kofunika kuti akhristu a mpingo wakatolika ndi Orthodox mdziko la Syria akhale ndi mapemphero apadera opephelera mtendere wa ana.