Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Charity of Ottawa Ipempha Atsikana kuti Atumikire Mulungu Kudzera Mu Usisitere

$
0
0

Atsikana mu mpingo wakatolika awapempha kuti adzipereke ku moyo wotumikira Mulungu kudzera mu njira ya usisteri kuti nawo akhale zida zenizeni zothandizira pa ntchito yofalitsa uthenga wabwino ponseponse kudzera mu mpingowu.

Asisteli a chipani cha Charity Of Ottawa, omwe amadziwikanso ndi kuti Grey Nuns Of The Cross,  Sister Cecilia Kaononga anena izi polankhula ndi Radio Maria pa sukulu ya ukachenjede ya Catholic Unirvesity ku Nguludi m’boma la Chiradzulu.

“Tikuwapempha atsikana kuti alimbikire maphunziro komanso kupemphera. Akapemphera apemphe Mulungu awaunikire chimene akufuna pa moyo wawo,” anatero Sister Kaononga.

Iwo ati khomo la chipani chawo ndi lotsekula kotero kuti mtsikana aliyense amene akumva kuyitanidwa mu mu njira ya usisiteli asachedwe koma kulowa mu chipanichi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>