Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati pemphero lowona limachokera mu mtima mwa munthu amene amazindikira kulakwitsa kwake ndi kulapa.
Papa amalankhula izi pa bwalo la St Peters’s ku likulu la mpingowu ku Vatican pa mkumano omwe amakhala nawo lachitatu lililonse ndi anthu okayendera likulu la mpingowu ochokera mmaiko osiyanasiyana.
Papa wati Mulungu amachitira chifundo anthu a chilungamo komanso odzichepetsa.
Iye wati popemphera, akhristu akuyenera kutengera chitsanzo cha nyimbo yotamanda Mulungu yomwe amayi Maria anayimba, pomwe amakumana ndi msuweni wake Elizabeti kamba koti imakamba kuti Mulungu amachitira chifundo anthu odzichepetsa ndipo amamva mapemphero awo.