Anthu othawa kwao pafupifupi mazana awiri ndi makumi asanu (250) ati apulumitsidwa bwato lomwe anakwera litagubuduzika pa nyanja yaikulu ya Mediterranean m’dziko la Greece.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC mabwato anayi ngakhalenso ndege ndi zomwe zathandiza populumutsa anthuwa.
Malipoti ati kusintha kwa nyengo ndi komwe kwachititsa kuti chiwerengero cha ngozi za mtunduwu chipitilire kukwera.
Kafukufuku wa bungwe lowona za mgwirizano wa maiko a pa dziko lonse la United Nations-UN wati anthu othawa kwao oposera 2500omwe anali paulendo wopita m’maiko a ku Ulaya, afa msabatayi pa ngozi za pa madzi.