Akhristu a mpingo wakatolika awapempha kuti atengere chitsanzo cha kulimba mtima pa chikhristu chawo monga momwe anachitira Amalitiri 22 a ku Uganda polora kuphedwa kamba chikhulupiliro chawo.
Episkopi wa dayosizi ya Kiyinda Mityana m’dzikomo ambuye Joseph Anthony Zziwandi yemwe wanena izi pa mwambo wa misa ya chaka cha chokumbukira Amalitiri-wa omwe unachitikira ku malo oyera mu mpingowu a Namugongo omwe akupezeka mu mzinda wa Kampala m’dziko-mo .
Mwambo wa a malitiri wa chaka chino wachitika pa mutu woti “Chilungamo ndi chimene chidzakumasuleni.”
Ambuye-wa ati akhristu akuyenera kuima pa choona kamba koti ndi chimene chidzawamasule komanso kutukula dziko lonse.
Ku mwambowu kunafika atsogoleri ndi akhristu a mpingowu ochokera m’maiko osiyanasiyana kuphatikizaponso a kuno ku Malawi.