Sukulu ya ana omwe ali ndi vuto losamva ku Mary View m’boma la Chiradzuluyapempha anthu m’dziko muno kuti azidzipeleka pa ntchito yothandiza ana ndi sukuluyi.
Sister Monica Cham’munda omwe ndi m’modzi mwa akuluakulu pa sukuluyi ndi omwe anena izi pa mwambo wolandira thandizo kuchokera kwa akhristu a bungwe la mabanja achikhristu la Chistian Family Movement (CFM) ku St.Martin Parishku ChirimbamuArkidayosizi ya Blantyre.
Iwo ati sukuluyi imasowa zambiri kotero kuti anthu ali omasuka kufika ndi kuthandiza ntchito za pa sukuluyi.
“Ndikupempha anthu akufuna kwabwino kuti atithandize kumbali ya chakudya chifukwa tili ndi ana ambiri panopa. Podziwa kuti sukulu yathuyi ndi yaulere zinthu zimativuta kapezedwe kake,” anatero Sister Cham’munda.
Polankhulanso m’modzi mwa atsogoleri a bungwe la CFM ku St. Martin Parish ku Chirimba a Victor Muhula anati bungwe lawo lafika ndi thandizolo pofuna kuthandiza kuchepetsa ena mwa mavuto pa sukuluyo.
“Ife a bungwe la banja la chikhristu, potengera chitsanzo cha amai Maria omwe anayendera Elizabeti ifenso tinachiwona chinthu cha mtengo wapatali kuti tiwayendere anzathu a kuno ku Mary View titamva kuti kuno kuli mavuto ochuluka, akusowa zakudya, zovala ndi zinthu zina, tinabwera kuzacheza nawo kuwalimbikitsa komanso kuwagawira kangachepe komwe tili nako,” anatero a Muhula.
Iwo apemphanso anthu akufuna kwabwino amene ali ndi kuthekera kuti apite ndi thandizo lawo ku sukuluyi.