Lipoti lomwe nthambi yowona zakafukufuku pa sukulu ina ya ukachenjede mdziko la America yatulutsa lati chiwerengero cha akhristu a mpingo wakatolika padziko lonse chikukwera kwambiri maka mmaiko a mu Africa.
Lipotilo lati chiwerengerochi chakwera ndi 400 miliyoni padziko lonse kuyambira mchaka cha 1980.
Ilo lati ngakhale izi zili choncho chiwerengero cha akhristu amene akutsatira masakaramenti mumpingowu chikutsika.
Ndipo chifukwa cha kukwera kwa chiwerengero cha akhristuwa chiwerengero cha maparishi komanso ansembe chikuchepa.
Lipotili lati mpofunika kuti maanja alimbikitse ana kuvomera mautumiki osiyanasiyana mumpingowu ndicholinga choti akhristu adzithandizidwa mokwanira pankhani za masakaramenti.