Chitetezo cha dziko lino ati chingalimbikitsidwe ngati pali ubale wabwino pakati pa apolisi ndi anthu amalonda.
Wachiwiri kwa mkulu wa apolisi ya Bvumbwe , SupretendantMoses Katanda walankhula izi ndi Radio Maria kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo pambuyo pa mkumano wa apolisi ndi eni malo azisangalalo pa msika wa Bvumbwe.
Supretendant Katanda wati ntchito yolimbikitsa chitetezo ndi ya wina aliyense kotero pakufunika umodzi pogwira ntchitoyi.
“Tikupempha onse amalonda kuti tigwirane manja. Akawona anthu okaikitsa kumalo awo a malonda azitidziwitsa chifukwa nthawi zambiri anthu okuba kapena ochita zauchifwambawa amapezeka mmalo awo omwera mowa akudikilira kuti akachite zaupandu,” anatero Supretendent Katanda.
A Katanda apemphanso eni malo azisangalalo wa kuti azikhala ndi ziphaso zochitira malonda awo.