Amayi ampingo wakatolika mdziko muno awapempha akuti adzipeleke pa ntchito yokonzekera msonkhano wawo wapaziko lonse umene udzachike mwezi wa September m’dziko muno.
Msonkhanowu ndi wa amayi pa dziko lonse ndipo wakonzedwandibungwe loyimira amayiwa laWorld Union of Catholic Women Organisationndipo chaka chino awukonza kuti uchitikire mdziko muno.
Pofotokozera Radio Maria Malawi m’modzi mwa atsogoleri akale a bungweli mu arkidayosizi ya Blantyre,mayiEmily Kapeta,ati amayi mdziko muno akuyenara kutenga msonkhanowu ngati madalitso akululu kamba koti uyika pa mapu mbiri ya mpingowu mdziko muno.
“Msonkhano taukonzekera bwino ndipo tikuwulandira ndi manja awiri. Tikupempha amayi apitirizebe kupereka ma K200 kuti tikwanitse kukonzekera bwino msonkhano umenewu kuti uzayende bwino,” anatero mayi Chipeta.
Iwo ati kupatula ndalama zomwe amayiwa akupereka kuti izathandizire pa msonkhanowu, bungweli lakonza ulendo wandawala ndi cholinga chofuna kuwonjezera ndalamazi.
Aka kakhala koyamba kuti msonkhanowu uchitikire mdziko muno.