Bungwe la Eye ofthe Child m’dziko muno lalemba bukhu lomwe lili ndi mfundo zothandiza kuzindikira mavuto omwe ana amakumana nawo monga kugwililidwa mosavuta.
Polankhula ndi Radio Maria Malawi, mkulu wa bungweli m’dziko muno, a Maxwell Matewere, ati bungweli laganiza zotulutsa bukhuli ndi cholinga choti lithandize anthu mdziko muno kudziwa njira zoyenera kutsata kuti azitha kupereka chitetezo ndi chisamaliro chokwanira kwa ana kuti asamapezeke akukhudzidwa ndi mavuto ogwiliridwa amene akukolezera imfa zosiyanasiyana pakati pawo.
Iwo ati bukhuli alikhazikitsa lolemba pa 20 June mu m’zinda wa Lilongwe, mogwilizana ndi bungwe la FAWEMA ndipo mledo wolemekezeka ku mwambowu ndi mkazi wa mtsogoleri wa dziko lino mayi Getrude Mutharika.