Dziko la Malawi lachisanu lichita mwambo wa tsiku loganizira m’chitidwe woyipa wogwilitsa ntchito ana (World Day Against Child Labour).
Dziko la Malawi lidzachita mwambowu pogwilizana ndi mayiko pa dziko lonse. M’tsogoleri wa dziko lino Professor Peter Muthalika ndi amene adzatsogolere mwambo woganizira tsikuli omwe wakonzedwa kuti udzachitikire mu mzinda wa Lilongwe.
Mutu wa chaka chino woganizira tsikuli, ukulimbikitsa anthu m’dziko muno kuti adzipeleke pa ntchito zolimbana ndi m’chitidwe-wu, omwe ukuchitika m’mayiko pa dziko lonse.
Malingana ndi kalata yomwe a ku unduna wa za ntchito, achinyamata ndi zina, m’chitidwewu wafika pa 29% ukuchitika m’dziko muno, omwe ndi ma percent okwera kwambiri kusiyanasiyana momwe zinthu zikukhalira m’mayiko ena.
Bungwe lowona za antchito, la International Labour Organisationndi lomwe linakhadzikitsa tsikuli pofuna kulimbikitsa mayiko pa ntchito zolimbana ndi m’chitidwewu komanso kuwonetsetsa kuti ana akulandira chisamaliro ndi chitetezo chokwanira.