Mfumu Kachule ya m’dera la mfumu yayikulu Kachere m’boma laDedza yati ipitiliza kudzipeleka pa chisamaliro ndi chitetezo cha ana a m’dera lake ndi cholinga choti azikhala ndi kukula ndi makhalidwe abwino.
Mfumu-yi yanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pamene inafika ndi kudela-li.
Mfumuyi yati zina mwa zomwe ikuchita polimbikitsa makhalidwe a tsogolo labwino kwa anawa ndi monga kuwalimbikitsa za ubwino wa maphunziro, komanso kulumikizana ndi makolo kuti asamalore anawa kupezeka m’malo omwera mowa.
“Ndimalimbikitsa kuti ana asukulu mdera langa asamapezeke mmalo omwera mowa komanso kuti azikhala olimbikira sukulu. Makolo ndimawauza kuti tithandizane pancthitoyi chifukwa mphunzitsi wamkulu ndi kholo,” anatero Mfumu Kachule.