Mlembi watsopano wabungwe la maepiskopi mdziko muno la Episcopal conference of Malawi Bambo Henry Saindi ati apitiliza kudzipereka potumikira Mulungu pogwiritsa ntchito mphatso zomwe ali nazo pofunanso kuthandiza anthu ena kupyolera muudindo womwe asankhidwa.
Bambo Saindi anena izi lero polankhula ndi Radio Maria Malawi yomwe imafuna kumva momwe iwo awulandilira udindowu.
Iwo ati nthawi zina anthu amaganiza kuti kukhala paudindo waukulu ndi chiphinjo pa moyo wa munthu ,koma iwo ati nkhani ya udindo amaiwonera mbali ziwiri mbali yoyamba ndichinthu cholemela pamene mbali ina tintha kuwona udindo ngati mwayi umene munthu walandila ndicholinga choti atenge nawo mbali awonese mphatso imene ali nayo ponthandidza anthu ena ponthandidza mpingo komanso mbali zina.
“Ine poyamba ndikufuna kuthokoza Mulungu amene kupyolela Mbungwe la Episcopal Conference of Malawi wandiona kuti ndine woyenela kunkhala pa udindo umenewu”.
Iwo anapitilidza kunena kuti ngati tichita bwino ndi Mulungu amene amatinthandidza kuti tikwanilise, ndipo ndimulungu yemweyo wandiyetsa kuti ndine woyenela.
Kalata yotsimikiza Bambo Henry Saindi kunkhala Mlembe wa bungweri yatuluka lachinayi.