Bungwe la Technical Interprenual Vocational Education and Training Authority (TIVETA) lati ntchito yake yotolera misonkho iyamba kuyenda bwino kaamba ka mgwirizano omwe bungweli wasayinirana ndi bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA).
M’modzi mwa akuluakulu a bungweli a Willison Makulumiza Nkhoma alankhula izi lachinayi ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Lilongwe pomwe mabungwe awiriwa amasayinirana mgwirizanowu.
Iwo ati mgwirizanowu uthandiza kufikira anthu ambiri mdziko muno omwe amayenera kupereka misonkho ku bungwe lawo.
“A MRA akamatolera ndalama aziika ndalama zija mu account yathu ndipo ifeyo ndi amene tili ndi mphamvu yokachotsamo ndalama zija osati MRA,” anatero a Nkhoma.
Poyankhulaponso m’modzi mwa akuluakulu ku bungwe lotolera msonkho mdziko muno la Malawi Revenue Authority (MRA), a Steven Kapoloma anati bungwe lawo pa mgwirizano umenewu ntchito yake ndi yongotolera msonkho m’malo mwa bungwe la TIVETA.
“Pamene tagwirizana kuti ife a MRA tizitolera msonkho m’malo mwa iwo (TIVETA)udindo wathu wagona poonetsetsa kuti wolemba ntchito aliyense abwere ku MRA kudzalembetsa msonkho ndi kuyamba kulipira msonkho wa dziko. Chinanso ndichowadziwitsa kuti aphunzire kumawonkhetsa okha msonkho umenewu wa TIVETA,” anatero a Kapoloma.