Anthu omwe amagwira ntchito modzipereka ku Radio Maria Malawi awalimbikitsa kuti asamabwelere m’mbuyo pomwe akukumana ndi zovuta pa nthawi yomwe akutumikira.
Bambo Edwin Lambulira alankhula izi loweruka pambuyo pa m’bindikiro wa anthu omwe amatumikira ku likulu la wailesiyi ku Mangochi omwe unachitikira ku malo ogona alendo a Namiyasi mu dayosizi ya Mangochi ya mpingo wakatolika.
Iwo ati pa nthawi yomwe akukumana ndi zovuta akuyenera kupemphera kwa Mulungu kuti awatsogolele komanso kuwapatsa chilimbikitso.
“Nthawi zambiri anthu otumikira Mulungu akakumana ndi chinthu choti samachiyembekezera amabwelera m’mbuyo choncho ndinawona kuti ndikwabwino kuti tithandizane popemphera pa tsiku la lero. Ndawapempha kuti zisathere pakulankhula chabe koma azichite ndithu choncho azabala zipatso zochuluka,” anatero bambo Lambulira.
Pamenepa Bambo Lambulira apempha atumikiwa kuti nthawi zonse pamene akufalitsa uthenga wabwino kudzera pa wailesi, iwonso aziwonetsa chitsanzo chabwino kwa ena.
M’modzi mwa achinyamata otumikira ku Radio Maria Malawi yemwe anachita nawo m’bindikirowu a Gabriel Brome anati aphunzilapo kuti pamene akupita kowulutsa mau azikhala atazikonzekera bwino komanso iwowo azikhala chitsanzo chenicheni cha zomwe akuyankhula pa wailesi.
M’bindikirowu unachitika pa mutu wakuti “Kodi nanga inuyo simuchokanso?” Mau ochokera pa Yohane mutu 6 ndime ya 59 kulekezera 69.