Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisko anapempha mphindi yokhala chete pofuna kuyikiza mmapemphero anthu onse omwe akhudzidwa ndi chiwembu chomwe chachitika pa bwalo lina la ndege mu mzinda wa Istanbul mdziko la Turkey.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Papa anachita izi lero ndi alendo omwe amakayendera likulu la mpingowu omwe amasonkhana nawo lachitatu lililonse.
Papa anati awayikiza mmapemphero anthu onse omwe akhudzidwa pa chiwembuchi ngakhalenso mabanja awo.
Malipoti ati padakali pano chiwerengero cha anthu omwe afa powomberedwa ngakhalenso ndi mabomba omwe anaphulitsidwa pa chiwembuchi ndi chokwana 41 ndipo ena 239 avulala ndipo ati gulu la zauchifwamba la Islamic State ndi lomwe lachita chiwembuchi.