Dziko la Turkey lakhazikitsa tsiku la lachinayi pa 30 June, 2016 kukhala lapadera mdzikolo pofuna kukhudza maliro a anthu 42 omwe afa pa chiwembu chomwe chachitikira pa bwalo la ndege mu mzinda wa Istanbul mdzikolo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, zigawenga zomwe zachita chiwembuchi zitafika pamalowa zinayamba kuwombera anthuwa ndipo apolisi atalowelera ati zigawengazi zinaphulitsa mabomba omwe zinavala.
Malipoti ati anthu 239 ndi omwe avulala pa chiwembuchi ndipo mwa anthuwa 41 ati avulala modetsa nkhawa.
Padakali pano ati palibe gulu la zauchifwamba lomwe labwera poyera kuti ndi lomwe lachita chiwembuchi koma malipoti osatsimikizika akusonyeza kuti zigawenga za Islamic State zikukhudzidwa ndi chiwembuchi.