Pali chiyembekezo chakuti mwambo wotsekera Radio Maria Mariatona ku phiri la Michiru ku Arkdayosizi ya Blantyre ya mpingo wakatolika loweruka ukhala wopambamba kamba koti zonse zokonzera tsikuli ati zili mchimake.
Mlembi wa bungwe la abwenzi a Radio Maria Malawi ku arkidayosizi ya Blantyre ndi Chikwawa a Elia Jenela alankhula izi ndi Radio Maria Malawi yomwe imafuna kudziwa za dongosolo lomwe lakonzedwa pa tsikuli.
A Jenala apempha abwezi ndi akhristu akufuna kwabwino kuti azafike ku mwambowu kamba koti kukakhala zochitika zosiyanasiyana kuphatikizapo nsembe ya ukalistiya yothokoza Mulungu.
“Tikupempha abwenzi komanso akhristu onse akufuna kwabwino azafike pa tsikuli ku Chilomoni. Tili ndi chikhulupiliro kuti zonse zizayenda bwino. Ngati pali ma balance onsewo azatha tsikuli ndipo 10 million imeneyi tizaikwanitsa.
Patsikuli accountant adzatiuza ndalama zonse zomwe zatoleredwa kuyambira tsiku limene tinatsegulira Mariatona mpaka pamene tikutsekera. Makwaya amene akakometse mwambowu ndi St. Bernadette ya ku Bangwe parish komanso St. Cecilia ya ku Chilomoni parishi. Mlendo wathu wolemekezeka ndi a Mark Katsonga Phiri,”anatero a Jenala.
Malinga ndi a Jenala, mwambowu ukayamba ndi kukwera phiri njira ya kolona ndipo kenako nsembe ya ukaristia yomwe adzatsogolere ndi bambo Mwinganyama mothandizana ndi a Director a Radio Maria Malawi bambo Joseph Kimu. Mkatikati mwa misayi mukakhala kudalitsa zinthu zosiyanasiyana zomwe anthu akabweretse monga madzi, mchere, kandulo, mafuta ndi zina ndipo pamapeto pa nsembe ya misayi pakakhala perekaniperekani.