Msonkhano waukulu wachiwiri wa pachaka wa ma episkopi a mpingo wakatolika mdziko muno watha lero ku likulu la mpingowu mu mzinda wa Lilongwe.
Polankhula ndi Radio Maria Malawi pambuyo pa msonkhanowu mlembi wamkulu wa bungwe la maepiskopi mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM), bambo Henry Saindi, ati pa mfundo zomwe maepiskopiwa akambirana alimbikitsa moyo wa banja la chikhristu mowunikiridwa ndi kalata ya apapa yotchedwa “Amoris Lactitia” yomwe inatulutsidwa pambuyo pa misonkhano iwiri ya maepiskopi ya sinodi ya mabanja.
Bambo Saindi ati maepiskopiwa apempha mabungwe akufuna kwabwino kuti athandize dziko lino ndi chakudya kaamba koti madera ambiri mdziko muno akukumana ndi vuto la njala.
Mwa zina ku msonkhanowu maepiskopiwa alandira malipoti kuchokera ku mabungwe akuluakulu a mpingowu. Msonkhanowu omwe unali wa masiku anayi unasonkhanitsa ma Episkopi onse a mdziko muno kuphatikizapo nthumwi ya apapa mmaiko a Malawi ndi Zambia Arch-bishop Julio Murat.