Pamene chisankho cha pulezidenti mdziko la Burundi chikuyembekezeka kuchitika lachiwiri, mtsogoleri wa dzikolo Pierre Nkurunziza ati akuyembekezeka kupambana pa chisankhochi zomwe zichititse kuti akhale pa ulamuliro wa dziko logawikana.
Malinga ndi malipoti a NEWS24 zipani zotsutsa ndi magulu omwe si aboma akana kutenga nawo mbali pachisankhocho ndipo ati zomwe achita a Nkurunziza ndi zotsutsana ndi malamulo komanso kuphwanya mgwirizano wa mtendere womwe unakhazikitsidwa mdzikolo mu chaka cha 2006 pambuyo pa nkhondo ya pachiweniweni yomwe inachitika mdzikolo.
Chisankhocho chomwe otsutsa akana kupikisana nawo ati kamba koti ndi chobera, Pulezidenti Nkuruzinza alibe wopikisana naye.
Mmodzi mwa akuluakulu otsutsa mdzikolo wati boma la dzikolo ladzipatula kuti lichite chisankhocho litakanika kumvana pa zokambirana zodzetsa mtendere zomwe amachititsa mtsogoleri wa dziko la Uganda a Yoweri Museveni.