Bungwe losamalira ana la Chisomo Childrens Club lati lipitiriza kudzipereka polimbana ndi mchitidwe ozembetsa ana m'madera osiyanasiyana mdziko muno.
Bungweli lanena izi m’boma la Dedza pamsonkhano omwe bungweli linakonzera mafumu akuluakulu a m’bomalo pofuna kuwafotokozera zakuipa kwa mchitidwewu.Bungweli lati mafumu ali ndi udindo waukulu pantchito yolimbana ndi mchitidwe wozembetsa ana,kaamba koti iwo ndi amene amakhala ndi anthu nthawi zonse.Mmawu ake mkulu owona kuti palibe kusiyana pakati pa amuna ndi akazi pakagwiridwe ka ntchito kubungwe la Norwegian Church Aid Mai Habiba Osman,ati ndi zomvetsa chisoni poona kuti dziko lino, mpaka pano likadalibe lamulo lenileni komanso lokhazikika lolimbana ndi mchitidwewu