Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Kalindo Watula Pansi Udindo Wake

$
0
0

Phungu wa ku nyumba ya malamulo m’dera la kum’mwera mwa boma la Mulanje a Elias Bon Kalindo wati kutula pansi kwa udindo wake kuthandiza pa ntchito zopititsa luso la zisudzo mdziko muno.

A Kalindo alankhula izi ndi Radio Maria Malawi pamene imafuna kudziwa za tsogolo lawo pamene atula pansi udindo wawo ngati phungu wa ku nyumba ya malamulo wa chipani cha Democratic Progressive (DPP).

“Ndasiyadi udindo umenewu pa zichifukwa za ine mwini. Ndikufuna ndipange sukulu komanso monga mukudziwa ine ndi wazisudzo ndiye ndikufuna ndiyambe kujambula mafilimu osatinso ma sewero ayi choncho izizi zikufunika kuti ndikhale ndi nthawi yokwanira.

Iwo atsimikizira mtundu wa a Malawi kuti zomwe achitazi sizikugwirizana mu njira ina iliyonse ndi ndale ndipo ati chilichonse chili bwino.

“A Malawi adziwe kuti izi sizikugwirizana ndi ndi nkhani za ndale kapena kuti pali kusemphana kulikonse pakati pa chipani changa ndi ine. Zonse zili bwino bwino palibe chovuta.

Iwo anati tsogolo lawo ndilowala ndipo ati ngakhale asiya udindo wawo ngati phungu waku nyumba ya malamulo iwo apitilirabe kukhala membala wa chipani cha Decratic Progressive (DPP).


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>